Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 1:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. AWA ndi mau amene Mose ananena kwa Israyeli wonse, tsidya la Yordano m'cipululu, m'cidikha ca pandunji pa Sufu, pakati pa Parani, ndi Tofeli, ndi Labani, ndi Hazeroti, ndi Di Zahabi.

2. Ulendo wace wocokera ku Horebe wofikira ku Kadesi Barinea, wodzera njira ya phiri la Seiri, ndiwo wa masiku khumi ndi limodzi.

3. Ndipo kunali, caka ca makumi anai, mwezi wakhumi ndi umodzi, tsiku loyamba la mweziwo, Mose ananena ndi ana a Israyeli, monga mwa zonse Yehova adamlamulira awauze;

4. atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basana, wakukhala m'Asitaroti, ku Edrei.

5. Tsidya lija la Yordano, m'dziko la Moabu, Mose anayamba kufotokozera cilamulo ici, ndi kuti.

6. Yehova Mulungu wathu ananena ndi ife m'Horebe, ndi kuti, Yakwanira nthawi yokhala inu m'phiri muno;

7. bwererani, yendani ulendo wanu ndi kumuka ku mapiri a Aamori, ndi koyandikizana nao, kucidikha, kumapiri, ndi kunsi ndi kumwela, ndi kumphepete kwa nyanja, dziko la Akanani, ndi Lebano, kufikira nyanja yaikuru Firate.

8. Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao.

9. Ndipo muja ndinanena ndi inu, ndi kuti, Sinditha ine kukunyamulani ndekha;

10. Yehova Mulungu wanu anakucurukitsani, ndipo taonani, lero mucuruka ngati nyenyezi za kumwamba.

11. Yehova Mulungu wa makolo anu, acurukitsire ciwerengero canu calero ndi cikwi cimodzi, nakudalitseni monga iye ananena nanu!

12. Ndikasenza bwanji ndekha kupsinya kwanu, ndi katundu wanu, ndi kulimbana kwanu?

13. Dzifunireni amuna anzeru, ndi ozindikira bwino, ndi odziwika mwa mafuko anu, ndipo ndidzawaika akhale akuru anu.

14. Pamenepo munandiyankha ndi kuti, Mau mwanenawa ndi abwino kuwacita.

15. Potero ndinatenga akuru a mapfuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akuru anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi asanu, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mapfuko anu.

16. Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wace, ndi mlendo wokhala naye.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 1