AWA ndi mau amene Mose ananena kwa Israyeli wonse, tsidya la Yordano m'cipululu, m'cidikha ca pandunji pa Sufu, pakati pa Parani, ndi Tofeli, ndi Labani, ndi Hazeroti, ndi Di Zahabi.