Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 7:9-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo ndinali nawe kuli konse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akuru ali pa dziko lapansi,

10. Ndipo ndidzaikira anthu anga Israyeli malo, ndi kuwaoka kuti akakhale m'malo ao a iwo okha, osasunthikanso. Ndipo anthu a mphulupulu sadzawabvutanso, monga poyamba paja,

11. monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israyeli; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.

12. Pamene masiku ako akadzakwaniridwa, ndipo iwe udzagona ndi makolo ako, Ine ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, imene idzaturuka m'matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace.

13. Iye adzamangira dzina langa nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa cimpando ca ufumu wace ku nthawi zonse.

14. Ndidzakhala atate wace, iye nadzakhala mwana wanga; akacita coipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;

15. koma cifundo canga sicidzamcokera iye, monga ndinacicotsera Sauli amene ndinamcotsa pamaso pako.

16. Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wacifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.

17. Monga mwa mau onse awa ndi monga mwa masomphenya onse awa, momwemo Natani analankhula ndi Davide.

18. Pomwepo Davide mfumu analowa, nakhalapansi pamaso pa Yehova; nati, Ine ndine yani, Yehova Mulungu, ndi banja langa ndi ciani kuti munandifikitsa pano?

19. Ndipo icinso cinali pamaso panu cinthu cacing'ono, Yehova Mulungu; koma munanenanso za banja la mnyamata wanu kufikira nthawi yaikuru irinkudza; ndipo mwatero monga mwa macitidwe a anthu, Yehova Mulungu!

20. Ndipo Davide adzaonjezanso kunenanso ndi Inuj pakuti mudziwa mnyamata wanu, Yehova Mulungu.

21. Cifukwa ca mau anu, ndi monga mwa mtima wanu, munacita ukuru wonse umene kuuzindikiritsa mnyamata wanu.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 7