Ndipo icinso cinali pamaso panu cinthu cacing'ono, Yehova Mulungu; koma munanenanso za banja la mnyamata wanu kufikira nthawi yaikuru irinkudza; ndipo mwatero monga mwa macitidwe a anthu, Yehova Mulungu!