Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 5:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pomwepo mafuko onse a Israyeli anabwera kwa Davide ku Hebroni, nalankhula nati, Taonani, ife ndife pfupa lanu ndi mnofu wanu.

2. Masiku anapitawo, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisrayeli kuturuka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israyeli, ndi kukhala mtsogoleri wa Israyeli,

3. Comweco akuru onse a Israyeli anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo mfumu Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide mfumu ya Israyeli.

4. Davide anali ndi zaka makumi atatu polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi anai.

5. Ku Hebroni anacita ufumu pa Yuda zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi; ndi ku Yerusalemu anacita ufumu pa Aisrayelionse ndi Ayuda omwe zaka makumi atatu mphambu zitatu.

6. Ndipo mfumu ndi anthu ace anamuka ku Yerusalemu kuyambana nao Ajebusi, nzika za dziko; ndiwo ananena kwa Davide ndi kuti, Sudzalowa muno, koma akhungu ndi opunduka adzakupitikitsa; ndiko kunena kuti, Davide sakhoza kulowa muno.

7. Cinkana anatero Davide anathyola linga la Ziyoni, lomwelo ndilo mudzi wa Davide.

8. Ndipo tsiku lija Davide anati, Ali yense akakantha Ajebusi, aponye m'madzi opuala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Cifukwa cace akuti, Akhungu ndi opuala sangalowe m'nyumbamo.

9. Ndipo Davide anakhala m'linga mula, nalicha mudzi wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.

10. Ndipo Davide anakula cikulire cifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 5