Masiku anapitawo, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisrayeli kuturuka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israyeli, ndi kukhala mtsogoleri wa Israyeli,