Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 3:20-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Abineri nafika kwa Davide ku Hebroni, ali ndi anthu makumi awiri. Ndipo Davide anawakonzera Abineri ndi anthu okhala naye madyerero.

21. Pomwepo Abined anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisrayeli onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Comweco Davide analawirana ndi Abineri, namuka iye mumtendere.

22. Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yoabu anabwera kucokera ku nkhondo yobvumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abineri sanali ku Hebroni kwa Davide, cifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere.

23. Tsono pofika Yoabu ndi khamu lonse anali nalo, ena anamfotokozera Yoabu nati, Abineri mwana wa Neri anabwera kwa mfumu, amene analawirana naye, namuka iye mumtendereo

24. Pomwepo Yoabu anadza kwa mfumu, nati, Mwacitanji? Taonani, Abineri anadza kwa inu, cifukwa ninji tsono munalawirana naye kuti acokedi.

25. Mumdziwa Abineri mwana wa Neri kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kuturuka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikucita inu.

26. Ndipo Yoabu anaturuka kwa Davide, natumizira Abineri mithenga, amene anambweza ku citsime ca Sira. Koma Davide sanacidziwa.

27. Pofikanso Abineri ku Hebroni, Yoabu anampambutsa kupita nave pakati pa cipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, cifukwa ca mwazi wa Asaheli mbale wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 3