Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 24:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israyeli, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israyeli ndi Yuda.

2. Ndipo mfumu inanena ndi Yoabu kazembe wa khamu, amene anali naye, Kayendere tsopano mafuko onse a Israyeli, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, nuwerenge anthuwo, kuti ndidziwe kucuruka kwao kwa anthu.

3. Ndipo Yoabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwacurukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu acione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi cinthu ici?

4. Koma mau a mfumu anapambana Yoabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yoabu ndi atsogoleri a khamulo anaturuka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israyeli.

5. Naoloka Yordano, namanga zithando ku Aroeri ku dzanja lamanja kwa mudzi uli pakati pa cigwa ca Gadi, ndi ku Jazeri;

6. nafika ku Gileadi ndi ku dera la Tatimuhodisi; nafika ku Dani-Jaana ndi kuzungulira, kufikira ku Zidoni,

7. nafika ku linga la Turo ndi ku midzi yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; naturukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba.

8. Comweco pamene atayenda dziko lonse anafika ku Yerusalemu pakutha miyezi isanu ndi inai, ndi masiku makumi awiri.

9. Ndipo Yoabu anapereka kwa mfumu kucuruka kwa anthu adawawerenga; ndipo m'lsrayeli munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu.

10. Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwoo Davide nati kwa Yehova, Ndinacimwa kwakukuru ndi cinthu cimene ndinacita; koma tsopano Yehova mucotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinacita kopusa ndithu.

11. Ndipo pouka Davide m'mawa mau a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlauli wa Davide, kuti,

12. Kalankhule ndi Davide, Atero Yehova, kuti, Ndikuikira zinthu zitatu; udzisankhire wekha cimodzi ca izo, ndikakucitire cimeneco.

13. Comweco Gadi anafika kwa Davide, namuuza, nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupitikitsani miyezi itatu? kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Cenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 24