Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 2:16-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzace, nagwaza ndi lupanga lace m'nthiti mwa mnzaceo Comweco anagwa limodzi; cifukwa cace malo aja anachedwa Dera la Mipeni la ku Gibeoni.

17. Ndipo tsikulo nkhondo inakula ndithu. Ndi Abineri ndi anthu a Israyeli anathawa pamaso pa anyamata a Davide.

18. Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yoabu, Abisai ndi Asaheli. Ndipo Asaheli anali waliwiro ngati nyama ya kuthengo.

19. Ndipo Asaheli anapitikitsa Abineri. Ndipo m'kuthamanga kwace sanapambukira kulamanja, kapena kulamanzere, pakutsata Abineri.

20. Pomwepo Abineri anaceuka nati, Kodi ndi iwe Asaheli? iye nayankha, Ndine.

21. Ndipo Abineri ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zace. Koma Asaheli anakana kupambuka pakumtsata iye.

22. Ndipo Abineri anabwereza kunena kwa Asaheli, Pambuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yoabu?

23. Koma iye anakana kupambuka; cifukwa cace Abineri anamkantha ndi khali la mkondo m'mimba mwace, ndi khalilo linaturuka kumbuyo kwace. Ndipo anagwako, nafera pomwepo, Ndipo onse akufika kumalo kumene Asaheli anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo.

24. Koma Yoabu ndi Abisai anampitikitsa Abineri; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku citunda ca Ama, cakuno ca Giya, pa njira ya ku cipululu ca Gibeoni.

25. Ndipo ana a Benjamini anaunjikana pamodzi kutsata Abinen, nakhala gulu limodzi, naima pamwamba pa citunda.

26. Pomwepo Abineri anaitana Yoabu nati, Kodi lupanga lidzaononga cionongere? sudziwa kodi kuti kutha kwace kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao?

27. Yoabu nati, Pali Mulungu, iwe ukadapandakunena, anthu akadabalalika m'mawa osatsata yense mbale wace.

28. Comweco Yoabu anaomba Gpenga, anthu onse naima, naleka kupitikitsa Aisrayeli, osaponyana naonso.

29. Ndipo Abineri ndi anthu ace anacezera usiku wonse kupyola cidikha, naoloka Yordano, napyola Bitroni lonse nafika ku Mahanaimu.

30. Ndipo Yoabu anabwerera pakutsata Abineri. Ndipo pamene anasonkhanitsa pamodzi anthu onse anasowa anthu a Davide khumi ndi asanu ndi anai ndi Asaheli.

31. Koma anyamata a Davide anakantha anthu a Benjamini ndi a Abineri, namwalira mazana atatu mphambu makumi asanu ndi limodzi.

32. Ndipo ananyamula Asaheli namuika m'manda a atate wace ali ku Betelehemu. Ndipo Yoabu ndi anthu ace anacezera kuyenda usiku wonse, ndipo kudawacera ku Hebroni.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 2