Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 19:32-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka cakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.

33. Ndipo mfumu inanena ndi Barizilai, Tiyeni muoloke nane, ndipo ndidzakusungani pamodzi ndi ine ku Yerusalemu.

34. Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kumka ku Yerusalemu?

35. Lero ndiri nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira cimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oyimba? Cifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu.

36. Mnyamata wanu angofuna kuoloka Yordano pamodzi ndi mfumu; ndipo afuniranji mfumu kundibwezerapo mphothoyotere?

37. Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mudzi wanga ku manda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Cimamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumcitire cimene cikukomerani.

38. Ndipo mfumu inayankha, Cimamu adzaoloka nane, ndipo ndidzamcitira cimene cikukomereni; ndipo ciri conse mukadzapempha kwa ine ndidzakucitirani inu.

39. Ndipo anthu onse anaoloka Yordano, ndi mfumu yomwe inaoloka; ndipo mfumuyo Inapsompsona Barizilai nimdalitsa; ndipo iye anabwerera kunka kumalo kwace.

40. Comweco mfumu inaoloka nifika ku Giligala, ndi Cimamu anaoloka naye, ndipo anthu onse a Yuda adaolotsa mfumu, ndiponso gawo lina la anthu a Israyeli.

41. Ndipo onani, Aisrayeli onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakucotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lace pa Yordano, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye?

42. Ndipo anthu onse a Yuda anayankha anthu a Israyeli. Cifukwa mfumu iri ya cibale cathu; tsono mulikukwiyiranji pa mrandu umenewu? tinadya konse za mfumu kodi? kapena kodi anatipatsa mtulo uli wonse?

43. Ndipo anthu a Israyeli anayankha anthu a Yuda, nati, Ife tiri ndi magawo khumi mwa mfumu, ndi mwa Davide koposa inu; cifukwa ninji tsono munatipeputsa ife, osayamba kupangana nafe za kubwezanso mfumu yathu? Koma mau a anthu a Yuda anali aukali koposa mau a anthu a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 19