Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 15:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, citapita ici Abisalomu anadzikonzera gareta ndi akavalo ndi anthu makumi asanu akuthamanga momtsogolera.

2. Ndipo Abisalomu analawirira, nakaima pa njira ya kucipata; ndipo kunatero, pakakhala munthu ali yense ndi mrandu woyenera kufika kwa mfumu kuti aweruze, Abisalomu anamuitana, nati, Ndinu wa ku mudzi uti? Ndipo anati, Mnyamata wanu; ndiye wa pfuko tina la Aisrayeli.

3. Abisalomu nanena naye, Ona zokamba zako ndizo zabwino ndi zolungama; koma mfumu sinauze wina kuti adzamve za iwe.

4. Abisalomu anatinso, Mwenzi atandiika ine ndikhale woweruza m'dzikomo, kuti munthu yense amene ali ndi mrandu wace kapena cifukwa cace, akadafika kwa ine; ndipo ndikadamcitira zacilungamo!

5. Ndipo kunatero kuti pakusendera munthu ali yense kudzamlambira, iye anatambasula dzanja lace, namgwira, nampsompsona.

6. Abisalomu anacitira zotero Aisrayeli onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mrandu wao; comweco Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israyeli.

7. Ndipo kunali pakutha zaka zinai Abisalomu ananena kwa mfumu, Mundilole ndimuke ku Hebroni ndikacite cowinda canga ndinaciwindira Yehova.

8. Pakuti mnyamata wanu ndinawinda pakukhala ine ku Gesuri m'Aramu, ndi kuti, Yehova akadzandibwezeranso ndithu ku Yerusalemu, ine ndidzatumikira Yehova.

9. Ndipo mfumu inanena naye, Muka ndi mtendere. Comweco ananyamuka, nanka ku Hebroni.

10. Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israyeli, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni.

11. Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m'kupulukira kwao, osadziwa kanthu.

12. Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofeli Mgiloni, mphungu wa Davide, ku mudzi wace ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo ciwembuco cinali colimba; pakuti anthu anacurukacurukabe kwa Abisalomu.

13. Ndipo mthenga unafika kwa Davide nuti, Mitima ya anthu a Israyeli itsata Abisalomu.

14. Ndipo Davide ananena nao anyamata ace onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kucoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mudzi ndi lupanga lakuthwa.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 15