Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 10:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali zitapita izi, mfumu ya ana a Amoni inamwalira, ndipo Hanuni mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

2. Ndipo Davide anati, Ndidzacitira Hanuni mwana wa Nahasi zokoma, monga atate wace anandicitira ine zokoma. Comweco Davide anatumiza ndi dzanja la anyamata ace kuti akamsangalatse cifukwa ca atate wace. Ndipo anyamata a Davide anafika ku dziko la ana a Amoni.

3. Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumiza anyamata ace kwa inu, kuti ayang'ane mudziwo ndi kuuzonda ndi kuupasula?

4. Comweco Hanuni anatenga anyamata a Davide nawameta ndebvu zao mbali imodzi, nadula zobvala zao pakati, kufikira m'matako ao, nawaleka amuke.

5. Pamene anaciuza Davide iye anatumiza anthu kukakomana nao; pakuti amunawo anacita manyazi akuru. Niti mfumu, Bakhalani ku Yeriko kufikira zamera ndebvuzanu; zitameramubwere.

6. Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Betirehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu cikwi cimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.

7. Ndipo pamene Davide anacimva, anatumiza Yoabu ndi khamu lonse la anthu amphamvu.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 10