Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 34:2-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Nacita zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira za Davide kholo lace, osapambuka ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.

3. Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lace; ndipo atakhala zaka khumi ndi cimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzicotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga,

4. Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pace; nawalikha mafano a dzuwa anakwezeka pamwamba pao; naphwanya zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga; nazipera, naziwaza pamanda pa iwo amene adaziphera nsembe.

5. Napsereza mafupa a ansembe pa maguwa a: nsembe ao, nayeretsa Yuda ndi Yerusalemu.

6. Nateronso m'midzi ya Manase, ndi Efraimu, ndi Simeoni, mpaka Nafitali, m'mabwinja mwao mozungulira.

7. Nagumula maguwa a nsembe, naperapera zifanizo ndi mafano osema, nalikha mafano a dzuwa onse m'dziko lonse la Israyeli, nabwerera kumka ku Yerusalemu.

8. Atakhala mfumu tsono zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri, atayeretsa dziko ndi nyumbayi, anatuma safana mwana wa Azaliya, ndi Maseya kazembe wa mudzi, ndi Yona mwana wa Yoadazi wolemba mbiri, akonze nyumba ya Yehova Mulungu wace.

9. Ndipo anadza kwa Hilikiya wansembe wamkulu, napereka ndarama adabwera nazo ku nyumba ya Mulungu, zimene Alevi osunga pakhomo adasonkhanitsa kuzilandira ku dzanja la Manase ndi Efraimu, ndi kwa otsala onse a Israyeli, ndi kwa Yuda yense, ndi Benjamini, ndi kwa okhala m'Yerusalemu.

10. Ndipo anazipereka m'dzanja la anchito oikidwa ayang'anire nyumba ya Yehova; ndi iwo anazipereka kwa anchito akucita m'nyumba ya Yehova, kukonza ndi kulimbitsa nyumbayi;

11. anazipereka kwa amisiri a mitengo ndi omanga nyumba, agule miyala yosema, ndi mitengo ya mitanda yam'mwamba ndi yammunsi ya nyumbazi, adaziononga mafumu a Yuda.

12. Ndipo amunawo anacita nchitoyi mokhulupirika; ndi oikidwa awayang'anire ndiwo Yohati ndi Obadiya, Alevi, a ana a Merari; ndi Zekariya ndi Mesulamu, a ana a Akohati, kuifulumiza; ndi Alevi ena ali yense wa luso la zoyimbira,

13. Anayang'aniranso osenza akatundu, nafulumiza onse akugwira nchito ya utumiki uli wonse; ndi mwa Alevi munali alembi, ndi akapitao, ndi odikira.

14. Ndipo pakuturutsa ndarama zimene adalowa nazo ku nyumba ya Yehova, Hilikiya wansembe anapeza buku la cilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.

15. Ndipo Hilikiya anayankha nati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la cilamulo m'nyumba ya Yehova. Hilikiya napereka buku kwa Safani.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 34