Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 7:8-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m'hema mmodzi, nadya namwa, natengako siliva ndi golidi ndi zobvala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m'hema mwina, natengako, namuka, nazibisa.

9. Pamenepo ananenana wina ndi mnzace, Sitirikucita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tirikukhala cete; tikacedwa kufikira kwaca, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m'nyumba ya mfumu.

10. Nadza iwo, naitana mlonda wa mudzi, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi aburu omanga, ndi mahema ali cimangire.

11. Ndipo iye anaitana alonda ena, ndi iwo anafotokozera a m'nyumba ya mfumu.

12. Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ace, Ndikufotokozereni m'mene Aaramu aticitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, laturuka m'misasa, nabisala kuurengo, ndi kuti, Pamene aturuka m'mudzi tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m'mudzimo.

13. Nayankha mmodzi wa anyamata ace, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m'mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israyeli otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israyeli otsirizika; tiwatumize tione.

14. Motero anatenga magareta awiri ndi akavalo ao; ndipo mfumu inawatumiza alondole khamu la Aaramu, ndi kuti, Mukani mukaone.

15. Ndipo anawalondola mpaka ku Yordano; ndipo taonani, m'njira monse munadzala ndi zobvala ndi akatundu adazitaya Aaramu m'kufulumira kwao. Nibwera mithenga, nifotokozera mfumu.

16. Naturuka anthu, nafunkha m'misasa ya Aaramu. Ndipo anagula miyeso wa ufa ndi sekeli, nagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, monga umo adanenera Yehova.

17. Koma mfumu idayang'anitsa pacipata kazembe amene uja idafotsamira pa dzanja lace; ndipo anthu anampondereza pacipata, nafa iye, monga umo adanenera munthu wa Mulungu, ponena paja anamtsikira mfumu.

18. Ndipo kunacitika, monga adanena munthu wa Mulungu kwa mfumu, ndi kuti, Adzagula miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, adzagulanso muyeso wa ufa ndi sekeli; kudzatero mawa, dzuwa lino, pa cipata ca Samariya;

19. ndipo kazembe uja adayankha munthu wa Mulunguyo, nati, Taonani tsono, Yehova angacite mazenera m'mwamba, cikacitika ici kodi? Nati iye, Taona, udzaciona ici ndi maso ako, koma osadyako ai;

20. kudamcitikira momwemo; popeza anthu anampondereza pacipata nafa iye.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 7