Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 7:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Elisa anati, Mverani mau; a Yehova; atero Yehova, Mawa dzuwa lino adzagula muyeso wa ufa ndi sekeli, adzagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, pa cipata ca Samariya.

2. Pamenepo kazembe amene mfumu adafotsamira pa dzanja lace anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angacite mazenera m'mwamba cidzacitika ici kodi? Nati iye, Taona, udzaciona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.

3. Koma polowera pa cipata panali amuna anai akhate, nanenana wma ndi mnzace, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?

4. Tikati, Tilowe m'mudzi, m'mudzi muli njala, tidzafa m'mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa.

5. Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pace pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.

6. Popeza Yehova adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magareta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikuru; nanenana wina ndi mnzace, Taonani mfumu ya Israyeli watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aaigupto, atigwere.

7. Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi aburu ao, misasa iri cimangire; nathawa, apulumutse moyo wao.

8. Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m'hema mmodzi, nadya namwa, natengako siliva ndi golidi ndi zobvala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m'hema mwina, natengako, namuka, nazibisa.

9. Pamenepo ananenana wina ndi mnzace, Sitirikucita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tirikukhala cete; tikacedwa kufikira kwaca, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m'nyumba ya mfumu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 7