Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 6:7-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Nati, Katole. Natambasula dzanja lace, naitenga.

8. Ndipo mfumu ya Aramu inalinkucita nkhondo ndi Israyeli, nipangana ndi anyamata ace, kuti, Misasa yanga idzakhala pakuti pakuti.

9. Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Mucenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko.

10. Pamenepo mfumu ya Israyeli inatumiza kumene munthu wa Mulungu anamuuzako ndi kumcenjeza; nadzisunga osapitako, kawiri kawiri.

11. Koma mtima wa mfumu ya Aramu unabvutika kwambiri pa icico, naitana anyamata ace, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wobvomerezana ndi mfumu ya Israyeli ndani?

12. Nati mmodzi wa anyamata ace, lai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israyeli, ndiye amafotokozera mfumu ya Israyeli mau muwanena m'kati mwace mwa cipinda canu cogonamo.

13. Nati iye, Kamuoneni komwe ali; ndikatume munthu kumtenga. Ndipo anamuuza kuti, Ali ku Dotana.

14. Pamenepo anatumizako akavalo ndi magareta ndi khamu lalikuru, nafikako usiku, nauzinga mudziwo.

15. Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, naturuka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mudzi ndi akavalo ndi magareta. Ndi mnyamata wace ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! ticitenji?

16. Nati iye, Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife acuruka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.

17. Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ace kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magareta amoto akumzinga Elisa.

18. Ndipo atatsikira pali iye, Elisa anapemphera kwa Yehova, nati, Mukanthe mtundu uwu ucite khungu. Ndipo iye anawakantha, nawacititsa khungu, monga mwa mau a Elisa.

19. Ndipo Elisa ananena nao, Ngati njira ndi iyi? ngati mudzi ndi uwu? munditsate ine, ndidzakufikitsani kwa munthu mumfunayo; nawatsogolera ku Samariya.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 6