Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, naturuka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mudzi ndi akavalo ndi magareta. Ndi mnyamata wace ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! ticitenji?