Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 10:4-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Koma anaopa kwambiri, nati, Taonani, mafumu awiri sanaima pamaso pace, nanga ife tidzaima bwanji?

5. Ndipo iye wakuyang'anira nyumba, ndi iye wakuyang'anira mudzi, ndi akulu akulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzacita; sitidzalonga munthu yense mfumu; cokomera pamaso panu citani.

6. Nawalembera kalata kaciwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu va amunawo ana a mbuyewanu, ndi kundidzera ku Yezreeli mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mudzi, amene anawalera.

7. Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m'mitanga, naitumiza kwa iye ku Yezreeli.

8. Nudza mthenga, numfotokozera, kuti, Abwera nayo mitu va ana a mfumu. Nati iye, Mulunjike miulu iwiri polowera pa cipata kufikira m'mawa.

9. Ndipo kunali m'ma wa, iye anaturuka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani?

10. Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba va Ahabu; pakuti Yehova wacita cimene adanena mwa mtumiki wace Eliya.

11. Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu m'Yezreeli, ndi omveka ace onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ace, mpaka sanatsala wa iye ndi mmodzi yense.

12. Pamenepo ananyamuka, nacoka, namuka ku Samariya, Ndipo pokhala ku nyumba yosengera ya abusa panjira,

13. Yehu anakomana nao abale a Ahaziya mfumu ya Yuda, nati, Ndinu ayani? Nati iwo, Ife ndife abale a Ahaziya, tirikutsika kulankhulira ana a mfumu, ndi ana a nyumba yaikuru.

14. Nati iye, Agwireni amoyo. Nawagwira amoyo, nawapha ku dzenje la nyumba yosengera, ndiwo amuna makumi anai mphambu awiri; sanasiya ndi mmodzi yense.

15. Atacoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamcingamira; namlankhula, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga ubvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lace, namkweretsa pali iye pagareta.

16. Nati iye, Tiye nane, ukaone cangu canga ca kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'gareta wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 10