Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 10:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Atacoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamcingamira; namlankhula, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga ubvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lace, namkweretsa pali iye pagareta.

16. Nati iye, Tiye nane, ukaone cangu canga ca kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'gareta wace.

17. Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu m'Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Elisa.

18. Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi, nanena nao, Ahabu anatumikira Baala pang'ono, koma Yehu adzamtumikira kwambiri.

19. Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ace onse, asasowe mmodzi; pakuti ndiri nayo nsembe yaikuru yocitira Baala; ali yense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Kama Yehu anacicita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala.

20. Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira.

21. Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisrayeti onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m'nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala pha.

22. Nati kwa iye wosunga nyumba ya zobvala, Turutsira otumikira Baala onse zobvala. Nawaturutsira zobvala.

23. Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m'nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha.

24. Nalowa iwo kupereka nsembe zophera ndi nsembe zopsereza. Koma Yehu adadziikira kubwalo amuna makumi asanu ndi atatu, nati, Munthu akalola wina wa anthuwa ndirikuwaika m'manja mwanu apulumuke, moyo wace kulipa moyo wace.

25. Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asaturuke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka ku mudzi wa nyumba ya Baala.

26. Naturutsa zoimiritsa zija zinali m'nyumba ya Baala, nazitentha.

27. Nagamula fane la Baala, nagamula nyumba ya Baala, naiyesa dzala mpaka lero lino.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 10