Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 9:5-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamene anafika ku dziko la Zufi, Sauli anamuuza mnyamata amene anali naye, kuti, Tiye tibwerere; kuti atate wanga angaleke kusamalira aburuwo, ndi kutenga nkhawa cifukwa ca ife.

6. Koma ananena naye, Onatu, m'mudzi muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amcitira ulemu; zonse azinena zicitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tirikuyendera.

7. Ndipo Sauli ananena ndi mnyamata wace, Koma taona, tikapitako nmtengere ciani munthuyo? popeza mkate udatha m'zotengera zathu, ndiponso tiribe mphatso yakumtengera munthu wa Mulungu, tiri naco ciani?

8. Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Sauli nati, Onani m'dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wa siliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu.

9. Kale m'Israyeli, munthu akati afunse kwa Mulungu, adafotero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wochedwa mneneri makono ano, anachedwa mlauli kale.

10. Pamenepo Sauli anati kwa mnyamata wace, Wanena bwino; tiye tipite. Comweco iwowa anapita kumudzi kumene kunali munthu wa Mulunguyo.

11. Pakukwera kumudziko anapeza anthu akazi alikuturuka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?

12. Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumudzi kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;

13. mutafika m'mudzi, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Cifukwa cace kwerani; popeza nthawi yino mudzampeza.

14. Ndipo iwowa anakwera kumudzi; ndipo m'mene analowa m'mudzimo, onani, Samueli anaturukira pali Iwo, kuti akakwere kumsanje.

15. Ndipo Yehova anaululiratu m'khutu la Samueli dzulo lace la tsiku limene Sauli anabwera, kuti,

16. Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wocokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israyeli, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.

17. Ndipo pamene Samueli anaona Sauli, Yehova anati kwa iye, Ona munthu amene ndinakuuza za iye! ameneyu adzaweruza anthu anga.

18. Pomwepo Sauli anayandikira kwa Samueli pakati pa cipata, nati, Mundidziwitse nyumba ya mlauliyo iri kuti.

19. Ndipo Samueli anayankha Sauli nati, Inendinemlauliyo. Kwera, batsogola kumsanje, pakuti mudzadya ndi ine lero; ndipo m'mawa ndidzakulola upite, ndi kukudziwitsa zonse ziri mumtima mwako.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 9