Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 26:15-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Davide nati kwa Abineri, Si ndiwe mwamuna weni weni kodi? ndani mwa Aisrayeli afanafana ndi iwe? Unalekeranji tsono kudikira mbuye wako, mfumuyo? pakuti anafika wina kudzaononga mfumu, mbuye wako.

16. Ici unacicita siciri cabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, cifukwa simunadikira mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi cikho ca madzi zinali kumutu kwace ziri kuti?

17. Ndipo Sauli anazindikira mau ace a Davide, nati, Ndi mau ako awa, mwana wanga Davide? Nati Davide, Ndi mau anga mfumu, mbuye wanga.

18. Nati iye, Cifukwa ninji mbuye wanga amalondola mnyamata wace? pakuti ndacitanji? kapena m'dzanja langa muli coipa cotani?

19. Cifukwa cace mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wace. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire copereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipitikitsa lero kuti ndisalandireko colowa ca Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu yina.

20. Cifukwa cace tsono, mwazi wanga usagwe pansi kutati ndi Yehova; pakuti mfumu ya Israyeli yaturuka kudzafuna nsabwe, monga munthu wosaka nkhwali pamapiri.

21. Pamenepo Sauli anati, Ndinacimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakucitiranso coipa, popeza moyo wanga unati wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukuru.

22. Davide nayankha, nati, Tapenyani lmkondo wa mfumu Abwere mnyamata wina kuutenga.

23. Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense cilungamo cace ndi cikhulupiriko cace, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalola kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova,

24. Ndipo onani, monga lero ndinasamalira ndithu moyo wanu, momwemo usamaliridwe ndithu moyo wanga pamaso pa Yehova, ndipo iye andipulumutse ku masautso onse.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 26