Pamenepo Sauli anati, Ndinacimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakucitiranso coipa, popeza moyo wanga unati wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukuru.