Pomwepo Sauli anati kwa Davide, Udalitsike iwe, mwana wanga Davide; udzacita ndithu camphamvu, nudzapambana. Comweco Davide anamuka, ndipo Sauli anabwera kwao.