Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 25:33-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. ndipo, kudalitsike kucenjera kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi, ndi kusabwezera cilango ndi dzanja la ine ndekha.

34. Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israyeli, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundicingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutaca kanthu konse, ngakhale mwana wamwamunammodzi.

35. Comweco Davide analandira m'dzanja lace zimene iye anamtengera; nanena naye, Ukwere kwanu mumtendere; ona, ndamvera mau ako, ndabvomereza nkhope yako.

36. Ndipo Abigayeli anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwace, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwace, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuza kanthu konse, kufikira kutaca.

37. Tsono m'mawa vinyo atamcokera Nabala, mkazi wace anamuuza zimenezi; ndipo mtima wace unamyuka m'kati mwace, iye nasanduka ngati mwala.

38. Ndipo kunali, atapita masiku khumi, Yehova anamkantha Nabala, nafa.

39. Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mrandu wa mtonzo wanga wocokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wace pa coipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala coipa cace. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigayeli, zakuti amtengere akhale mkazi wace.

40. Ndipo anyamata a Davide pakufika kwa Abigayeli ku Karimeli, analankhula naye, nati, Davide anatitumiza kwa inu, kukutengani, mukhale mkazi wace.

41. Ndipo iye ananyamuka, nawerama nkhope yace pansi, nati, Onani, mdzakazi wanu ali kapolo wakusambitsa mapazi a anyamata a mbuye wanga.

42. Ndipo Abigayeli anafulumira nanyamuka, nakwera pa bum, pamodzi ndi anamwali ace asanu akumtsata; natsatira mithenga ya Davide, nakhala mkazi wace.

43. Davide anatenganso Ahinoamu wa ku Yezreeli, ndipo onse awiri anakhala akazi ace.

44. Pakuti Sauli anapatsa Mikala, mwana wace, mkazi wa Davide, kwa Paliti mwana wa Loisi, wa ku Galimu.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 25