Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 23:6-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo kunali kuti Abyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lace.

7. Ndipo anthu anauza Sauli kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Sauli anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.

8. Ndipo Sauli anamemeza anthu onse kunkhondo, kuti atsikire ku Keila, kumangira misasa Davide ndi anthu ace.

9. Ndipo Davide anadziwa kuti Sauli analikulingalira zomcitira zoipa; nati kwa Abyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi.

10. Nati Davide, Yehova, Mulungu wa Israyeli, mnyamata wanu wamva zoona kuti Sauli afuna kudza ku Keila, kuononga mudziwo cifukwa ca ine.

11. Kodi amuna a ku Keila adzandipereka m'dzanja lace? Kodi Sauli adzatsikira ndithu, monga mnyamata wanu wamva? Yehova Mulungu wa Israyeli, ndikupemphani, muuze mnyamata wanu. Ndipo Yehova anati, Adzatsika.

12. Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Sauli? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.

13. Potero Davide ndi anyamata ace, ndiwo monga ngati mazana asanu ndi limodzi, ananyamuka, naturuka ku Keila, nayendayenda kuli konse adakhoza kuyendako. Ndipo anauza Sauli kuti Davide wapulumuka ku Keila; iye naleka kumtsata.

14. Ndipo Davide anakhala m'cipululu m'ngaka, nakhala m'dziko la mapiri m'cipululu ca Zifi. Ndipo Sauli anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereka m'dzanja lace.

15. Ndipo Davide anaona kuti Sauli adaturuka kudzafuna moyo wace; Davide nakhala m'cipululu ca Ziti m'nkhalango.

16. Ndipo Jonatani mwana wa Sauli ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lace mwa Mulungu.

17. Ndipo iye ananena naye, Usaopa; cifukwa dzanja la Sauli atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israyeli, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, icinso Sauli atate wanga acidziwa.

18. Ndipo awiriwo anapangana pangano pamaso pa Yehova; ndipo Davide anakhala kunkhalango, koma Jonatani anapita ku nyumba yace.

19. Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Sauli ku Gibeya, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango, m'phiri la Hakila. Umene Uri kumwera kwa cipululu?

20. Cifukwa cace mfumu, tsikani, monga umo mukhumbire m'mtima mwanu kutsika; ndipo kudzakhala kwathu kumpereka iye m'dzanja la mfumu.

21. Sauli nati, Mudalitsike inu kwa Yehova; cifukwa munandicitira ine cifundo.

22. Mukanitu kuti mukadziwitse ndithu, ndi kudziwa ndi kuona mbuto m'mene akhalitsa, ndi amene adamuona m'menemo; cifukwa anandiuza kuti iye acita mocenjera ndithu.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 23