Ndipo iye ananena naye, Usaopa; cifukwa dzanja la Sauli atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israyeli, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, icinso Sauli atate wanga acidziwa.