Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 22:4-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo anawatenga kumka nao pamaso pa mfumu ya Moabu; ndipo iwo anakhala naye nthawi yonse Davide anali ku lingalo.

5. Ndipo mneneri Gadi anati kwa Davide, Musamakhala m'lingamo; cokani, mulowe m'dziko la Yuda. Potero Davide anacokako, nafika ku nkhalango ya Hereti.

6. Pakumva Sauli kuti anadziwika Davide, ndi anthu ace akukhala naye, Sauti analikukhala m'Gibeya, patsinde pa mtengo wa kumsanje, m'dzanja lace munali mkondo wace, ndi anyamata ace onse anaimirira pali iye.

7. Ndipo Sauli anati kwa anyamata ace akuima comzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Jese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yamphesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana;

8. kuti inu nonse munapangana dwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Jese, ndipo palibe wilia wa inu wakundidtira cifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe?

9. Pamenepo Doegi wa ku Edomu, anaimirira ndi anyamata a Sauli, nayankha, nati, Ine ndinamuona mwana wa Jeseyo alikufika ku Nobi, kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubu.

10. Ndipo iye anamfunsira kwa Yehova, nampatsa cakudya, nampatsanso lupanga la Gotiate Mfilistiyo.

11. Pamenepo mfumu anatuma mthenga kukaitana Ahimeleki wansembeyo, mwana wa Ahitubu, ndi banja lonse la atate wace, ansembe a ku Nobi; ndipo iwo onse anafika kwa mfumu.

12. Ndipo Sauli anati, Imva tsopano iwe mwana wa Ahitubu. Nayankha iye, Ndine, mbuye wanga.

13. Ndipo Sauli anati kwa iye, Munapangana dwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Jese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe?

14. Ndipo Ahimeleki anayankha mfumu, nati, Ndipo ndani mwa anyamata anu onse ali wokhulupirika ngati Davide amene, mkamwini wa mfumu; wakuyenda mu uphungu wanu, nalemekezeka m'nyumba mwanu?

15. Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wace kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 22