Pakumva Sauli kuti anadziwika Davide, ndi anthu ace akukhala naye, Sauti analikukhala m'Gibeya, patsinde pa mtengo wa kumsanje, m'dzanja lace munali mkondo wace, ndi anyamata ace onse anaimirira pali iye.