Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 2:15-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaoce; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi.

16. Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, lai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda.

17. Ndipo zoipa za anyamatawo zinali zazikuru ndithu pamaso pa Yehova; pakuti anthu anaipidwa ndi nsembe ya Yehova.

18. Koma Samueli anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m'cuuno ndi efodi wabafuta.

19. Ndiponso amace akamsokera mwinjiro waung'ono, nabwera nao kwa iye caka ndi caka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wace kudzapereka nsembe ya pacaka.

20. Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wace, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m'malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao.

21. Ndipo Yehova anakumbukila Hana, naima iye, nabala ana amuna atatu, ndi ana akazi awiri. Ndipo mwanayo Samueli anakula pamaso pa Yehova.

22. Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ace anacitira Aisrayeli onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la cihema cokomanako.

23. Ndipo iye ananena nao, Mumacitiranji zotere? popeza ndirinkumva za macitidwe anu oipa kwa anthu onsewa.

24. Iai, ana anga, popeza mbiri imene ndirikuimva siri yabwino iai; mulikulakwitsa anthu a Yehova.

25. Munthu akacimwira munthu mnzace oweruza adzaweruza mrandu wace; koma ngati munthu acimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, cifukwa Yehova adati adzawaononga.

26. Ndipo mwanayo Samueli anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anamkomera mtima.

27. Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziulula kwa banja la kholo lako, muja anali m'Aigupto, m'nyumba ya Farao?

28. Kodi sindinasankhula iye pakati pa mafuko onse a Israyeli, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe pa guwa langa, nafukize zonunkhira, nabvale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatsa banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israyeli?

29. Nanga umaponnderezeranji nsembe yanga ndi copereka canga, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo ucitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisrayeli, anthu anga?

30. Cifukwa cace Yehova Mulungu wa Israyeli akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Cikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 2