Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 19:9-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo mzimu woipa wocokera kwa Yehova unali pa Sauli, pakukhala iye m'nyumba mwace, ndi mkondo wace m'dzanja lace; ndipo Davide anayimba ndi dzanja lace.

10. Ndipo Sauli anayesa kupyoza Davide kumphatikiza kukhoma ndi mkondowo; koma iye anadzilanditsa kucoka pamaso pa Sauli; ndipo analasa khoma; ndipo Davide anathawa napulumuka usiku uja.

11. Ndipo Sauli anatumiza mithenga ku nyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa.

12. Comweco Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka.

13. Ndipo Mikala anatenga cifanizo naciika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwace, nacipfunda zopfunda.

14. Ndipo pamene Sauli anatumiza mithenga kuti ikamgwire Davide, anati, iye alikudwala.

15. Ndipo Sauli anatumiza mithengayo kuti ikaone Davide, nati, Mumtengere iye pa kama wace, kuti ndidzamuphe.

16. Ndipopakulowamithengayo, onani, pakama pali cifanizo ndi mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwace.

17. Nati Sauli kwa Mikala, Wandinyengeranii comweci, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Sauli, iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe.

18. Comweco anathawa Davide, napulumuka, nafika kwa Samueli: ku Rama, namuuza zonse Sauli anamcitira. Ndipo iye ndi Samueli anakhala ku Nayoti.

19. Ndipo wina anauza Sauli, kuti, Onani Davide ali ku Nayoti m'Rama.

20. Ndipo Sauli anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samueli mkuru wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera-mithenga ya Sauli, ninenera iyonso.

21. Ndipo pamene anauza Sauli, iye anatumiza mithenga yina; koma iyonso inanenera. Ndipo Sauli anatumiza mithenga kacitatu, nayonso inanenera.

22. Pamenepo iyenso anamuka ku Rama, nafika ku citsime cacikuru ciri ku Seku, nafunsa Dati, Samueli ndi Davide ali kuti? Ndipo wina anati, Taonani, ali ku Nayoti m'Rama.

23. Ndipo anapita komweko ku Nayoti m'Rama; ndi mzimu wa Mulungu unamgwera iyenso; ndipo anapitirira, nanenera, mpaka anafika ku Nayoti m'Rama.

24. Ndiponso anabvula zobvala zace, naneneranso pamaso pa Samueli nagona wamarisece usana womwe wonse, ndi usiku womwe wonse. Cifukwa cace amati, Kodi Saulinso ali pakati pa aneneri?

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 19