Ndipo pamene anauza Sauli, iye anatumiza mithenga yina; koma iyonso inanenera. Ndipo Sauli anatumiza mithenga kacitatu, nayonso inanenera.