Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 14:6-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Jonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zace, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira nchito; pakuti palibe comletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.

7. Ndipo wonyamula zida zace ananena naye, Citani zonse ziri mumtima mwanu; palukani, onani ndiri pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu.

8. Ndipo Jonatani anati, Taona, ife tidzapita kunka kwa anthuwo, ndipo tidzadziu lula kwa iwo.

9. Akatero ndi ife kuti, Baimani kufikira titsikira kwa inu; tsono tidzaima m'malo mwathu, osakwera kwa iwo.

10. Koma akatero kuti, Kwerani kuno kwa ife, tsono tidzakwera; pakuti Yehova wawapereka m'manja mwathu; ndipo ici cidzatikhalira cizindikilo.

11. Ndipo onse awiri anadziulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikuturuka m'mauna m'mene anabisala.

12. Ndipo a ku kabomawo anayankha Jonatani ndi wonyamula zida zace, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Jonatani anauza wonyamula zida zace, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israyeli.

13. Ndipo Jonatani anakwera cokwawa, ndi wonyamula zida zace anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Jonatani, ndi wonyamula zida zace anawapha pambuyo pace.

14. Kuwapha koyambako, Jonatani ndi wonyamula zida zace, anapha monga anthu makumi awiri, monga ndime ya munda yolima ng'ombe ziwiri tsiku limodzi.

15. Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; comweco kunali kunthunthumira kwakukuru koposa,

16. Ndipo ozonda a Sauli ku Gibeya wa ku Benjamini anayang'ana; ndipo, onani, khamu la anthu linamwazikana, kulowa kwina ndi kwina.

17. Pamenepo Sauli ananena ndi anthu amene anali naye, Awerenge tsopano, kuti tizindikire anaticokera ndani. Ndipo pamene anawerenga, onani Jonatani ndi wonyamula zida zace panalibe.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 14