Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 13:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Sauli anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ufumu wace; nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.

2. Pamenepo Sauli anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israyeli; zikwi ziwiri za iwowa zinali ndi Sauli ku Mikimasi, ndi ku phiri la ku Beteli; ndi cikwi cimodzi anali ndi Jonatani ku Gibeya wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.

3. Ndipo Jonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ici. Ndipo Sauli analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri.

4. Ndipo Aisrayeli onse anamva kunena kuti Sauli anathyola kaboma ka Afilisti, ndi kuti Afilisti anyansidwa ndi Aisrayeli. Ndipo anthuwo anasonkhana kwa Sauli ku Giligala.

5. Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisrayeli, anali nao magareta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi cimodzi, ndi anthu akucuruka monga mcenga wa pa dooko la nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.

6. Pamene anthu a Israyeli anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.

7. Ndipo Ahebri ena anaoloka Yordano nafika ku dziko la Gadi ndi Gileadi; koma Sauli akali ku Giligala, ndipo anthu onse anamtsata ndi kunthunthumira.

8. Ndipo iye anatsotsa masiku asanu ndi awiri, monga nthawi anampanga Samueli; koma Samueli sanafika ku Giligala, ndipo anthu anabalalika namsiya Sauli.

9. Pamenepo Sauli anati, Andipatsire kuno nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika. Ndipo iye anapereka nsembe yopserezayo.

10. Ndipo kunali kuti pakutsiriza iye kupereka nsembe yopserezayo, pomwepo, onani, Samueli anafika. Ndipo Sauli anamcingamira kukamlankhula iye.

11. Ndipo Samueli anati, Mwacitanji? Nati Sauli, Cifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafika masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi;

12. cifukwa cace ndinati, Afilisti adzatitsikira pane pa Giligala, ndisanapembedze Yehova; potero ndinadzifulumiza, ndi kupereka nsembe yopsereza.

13. Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Munacita kopusa; simunasunga lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene iye anakulamulirani; mwenzi Yehova atakhazikitsa nthawi yino ufumu wanu, ukhale pa Israyeli nthawi yosatha.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 13