Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala cikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pace; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ace, cifukwa inu simunasunga cimene Yehova anakulamulirani.