Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 8:27-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Kodi Mulungu adzakhala ndithu pa dziko lapansi? Taonani, thambo ndi m'Mwambamwamba zicepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.

28. Koma muceukire pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lace, Yehova Mulungu wanga, kumvera kulira ndi kupempha kwace kumene kapolo wanu apempha pamaso panu lero;

29. kuti maso anu atsegukire nyumba yino usiku ndi usana, kumalo kumene munanenako, Dzina langa lidzakhala komweko; kuti mumvere pemphero limene adzapemphera kapolo wanu lolunjika kumalo kuno.

30. Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisrayeli, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.

31. Ngati munthu akacimwira mnzace, ndi lumbiro likaikidwa pa iye kumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira patsogolo pa guwa la nsembe lanu m'nyumba yino;

32. mverani Inu pamenepo m'mwambamo, ndipo citani, weruzani akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera cimo lace, ndi kulungamitsa wolungamayo kumbwezera monga cilungamo cace.

33. Ndipo anthu anu Aisrayeli akawakantha adani ao cifukwa ca kucimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, lodi kubvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m'nyumba muno;

34. pamenepo mverani Inu m'Mwambamo, ndi kukhululukira cimo la anthu anu Aisrayeli, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.

35. Pamene kumwamba kwatsekeka, ndipo kulibe mvula cifukwa ca kucimwira Inu, nakapemphera iwo molunjika kumalo kuno, ndi kubvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kusiya zoipa zao, pakuwasautsa Inu;

36. pamenepo mverani Inu m'Mwamba, ndi kukhululukira cimo la akapolo anu, ndi la, anthu anu Aisrayeli; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula pa: dziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale colowa cao.

37. M'dziko mukakhala odala, mukakhala mliri, mlaza, cinoni, dzombe, kapena kapuci, adani ao akawamangira misasa m'dziko la midzi yao, mukakhala mliri uti wonse, kapena nthenda;

38. tsono pempho ndi pembedzero liri lonse akalipempha munthu ali yense, kapena anthu anu onse Aisrayeli, pakuzindikira munthu yense cinthenda ca mtima wa iye yekha, ndi kutambasulira manja ace ku nyumba yino;

39. pamenepo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kucita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zace zonse, amene Inu mumdziwa mtima wace, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu;

40. kuti aope Inu masiku onse akukhala iwowo m'dziko limene Inu munapatsa makolo ao.

41. Ndiponso kunena za mlendo, wosati wa anthu anu Aisrayeli, koma wakufumira m'dziko lakutali cifukwa ca dzina lanu,

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 8