Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 7:18-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. M'mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nacita momwemo ndi mutu winawo.

19. Ndipo mituyi inali pamwamba pa nsanamira za pa likole inali ngati akakombo malembedwe ace, a mikono inai.

20. Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m'mbali mwace mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga nda nda mutu winawo.

21. Ndipo anaimiritsa nsanamirazi pa likole la Kacisi; naimiritsa nsanamira ya ku dzanja lamanja, nacha dzina lace Yakini; naimiritsa nsanamira yakumanzere, nacha dzina lace Boazi.

22. Ndipo pamwamba pa nsanamirazo panali ngati akakombo malembedwe ace; motero anaitsiriza nchito ya nsanamirazo.

23. Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwace kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wace unali mikono isanu; ndi cingwe ca mikono makumi atatu cinalizungulira.

24. Ndipo m'khosi mwace munali ngati zikho zozinganiza m'mkono umodzi zikho khumi zakuzinganiza thawalelo; zikhozo zinayengedwa m'mizere iwiri poyengedwa thawalelo.

25. Linasanjikika pa ng'ombe khumi mphambu ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, zitatu kumadzulo, zitatu kumwera, zitatu kum'mawa; ndipo thawalelo linakhazikika pamwamba pa izo; ndipo nkholo zao zinayang'anana.

26. Ndipo kucindikira kwace kunali ngati m'manja mwa munthu, ndipo mlomo wace unasadamuka ngati mlomo wa comwera, ngati maluwa akakombo, analowamo madzi a mitsuko yaikuru zikwi ziwiri.

27. Ndipo anapanga maphaka khumi amkuwa, m'litali mwace mwa phaka limodzi mikono inai, ndi kupingasa kwace mikono inai, ndi msinkhu wace mikono itatu.

28. Ndipo mapangidwe a maphakawo anali otere: anali nao matsekerezo ao, ndipo matsekerezo anali pakati pa mbano.

29. Ndipo pa matsekerezo a pakati pa mbano panali ngati mikango ndi ng'ombe ndi akerubi, ndi pamwamba pa mbano panali cosanjikirapo; ndipo pansi pa mikango ndi ng'ombe panaphatikizika zotsetseremba zoyangayanga zokoloweka.

30. Ndipo phaka lid lonse linali ndi njinga zamkuwa zinai ndi mitanda yamkuwa, ndipo ngondya zace zinai zinali ndi mapewa; pansi pa thawale panali mapewa oyengeka pa mbali pa zophatikizika zonse.

31. Ndipo pakamwa pace m'katimo pamwamba pa cosanjikira, panayesa mkono umodzi; koma pakamwa pace panali posadamuka, monga mapangidwe ace a cosanjikira, mkono umodzi ndi nusu; ndiponso pakamwa pace panali zolemba ndi matsekerezo ace anali amphwamphwa, si ozunguniza.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 7