Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 22:1-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Aaramu ndi Aisrayeli anakhala cete zaka zitatu, osathirana nkhondo.

2. Koma kunacitika caka cacitatu, kuti Yehosafati mfumu ya Yuda anatsikira kwa mfumu ya Israyeli.

3. Ndipo mfumu ya Israyeli ananena ndi anyamata ace, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Gileadi ngwathu, ndipo tangokhala cete, osaulanditsa m'dzanja la mfumu ya Aramu.

4. Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Gileadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israyeli, M'mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavale ako.

5. Ndipo Yehosafati ananena ndi mfumu ya Israyeli, Fuusira ku mau a Yehova lero.

6. Pamenepo mfumu ya Israyeli inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Gileadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu.

7. Koma Yehosafati anati, Kodi pano palibe mneneri wina wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?

8. Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wace wa Yimla. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.

9. Tsono mfumu ya Israyeli anaitana mdindo, nati, Kamtenge msanga Mikaya mwana wa Yimla.

10. Ndipo mfumu ya Israyeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wacifumu wace, obvala zobvala zao zacifumu pabwalo pa khomo la cipata ca Samaria; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao.

11. Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zacitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti,

12. Ndipo aneneri onse ananena momwemo, nati, Kwerani ku Ramoti Gileadi, ndipo mudzacita mwai; popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.

13. Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri abvomerezana zokoma kwa mfumu ndi m'kamwa m'modzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino.

14. Koma Mikaya anati, Pali Yehova, zimene Yehova adzanena nane ndidzanena ine.

15. Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Gileadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzacita mwai, popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.

16. Ndipo mfumu inati, Ndikulumbiritse kangati kuti undiuze zoona zokha zokha m'dzina la Yehova?

17. Nati iye, Ndinaona Aisrayeli onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi ziribe mwini, yense abwerere ndi mtendere ku nyumba yace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 22