Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Gileadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzacita mwai, popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.