Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wace wa Yimla. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.