Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 21:3-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni colowa ca makolo anga,

4. Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwace wamsunamo ndi wokwiya, cifukwa ca mau amene Naboti wa ku Yezreeli adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani colowa ca makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wace, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate.

5. Koma Yezebeli mkazi wace anadza kwa iye, nati kwa iye, Mucitiranji msunamo, kuti mukana kudya mkate?

6. Nati kwa iye, Popeza ndinalankhula kwa Naboti wa ku Yezreeli, ndinati kwa iye, Undigulitse munda wako ndi ndalama; kapena ukafuna, ndikupatsa munda wina m'malo mwace; kama anandiyankha, Sindikupatsani munda wanga wamphesa.

7. Ndipo Yezebeli mkazi wace anati kwa iye, Kodi mulamulira Aisrayeli tsopano ndinu? Taukani, idyani mkate, ukondwere mtima wanu; munda wa Naboti wa ku Yezreeli ndidzakupatsani ndine.

8. M'mwemo analemba akalata m'dzina la Ahabu nakhomerapo cizindikilo cace, natumiza akalatawo kwa akulu ndi omveka anali m'mudzi mwace, nakhala naye Naboti.

9. Ndipo analemba m'akalata, nati, Lalikirani kuti asale kudya, muike Naboti pooneka ndi anthu;

10. ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pace, kuti amcitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumturutse ndi kumponya miyala kumupha.

11. Ndipo anthu aja a mudzi wace, ndiwo akulu ndi omveka adakhala m'mudzi mwace, anacita monga Yezebeli anawatumizira, monga munalembedwa m'akalata amene iye anawatumizira.

12. Analalikira kuti asale kudya, naike Naboti pooneka ndi anthu.

13. Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pace, ndipo anthu oipawo anamcitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamturutsa m'mudzi, namponya miyala, namupha.

14. Pomwepo anatuma mau kwa Yezebeli, nati, Naboti waponyedwa miyala, nafa.

15. Ndipo kunali, atamva Yezebeli kuti anamponya Naboti miyala nafa, Yezebeli anati kwa Ahabu, Taukani, landirani munda wamphesa wa Naboti Myezreeli uja anakana kukugulitsani ndi ndarama, popeza, Naboti sali ndi moyo, koma wafa.

16. Ndipo kunali, atamva Ahabu kuti Naboti wafa, Ahabu anauka kukatsikira ku munda wamphesa wa Naboti, kuulandira.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 21