Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 21:10-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pace, kuti amcitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumturutse ndi kumponya miyala kumupha.

11. Ndipo anthu aja a mudzi wace, ndiwo akulu ndi omveka adakhala m'mudzi mwace, anacita monga Yezebeli anawatumizira, monga munalembedwa m'akalata amene iye anawatumizira.

12. Analalikira kuti asale kudya, naike Naboti pooneka ndi anthu.

13. Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pace, ndipo anthu oipawo anamcitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamturutsa m'mudzi, namponya miyala, namupha.

14. Pomwepo anatuma mau kwa Yezebeli, nati, Naboti waponyedwa miyala, nafa.

15. Ndipo kunali, atamva Yezebeli kuti anamponya Naboti miyala nafa, Yezebeli anati kwa Ahabu, Taukani, landirani munda wamphesa wa Naboti Myezreeli uja anakana kukugulitsani ndi ndarama, popeza, Naboti sali ndi moyo, koma wafa.

16. Ndipo kunali, atamva Ahabu kuti Naboti wafa, Ahabu anauka kukatsikira ku munda wamphesa wa Naboti, kuulandira.

17. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Eliya waku Tisibe, nati,

18. Nyamuka, tsikira kukakomana ndi Ahabu mfumu ya Israyeli, akhala m'Samariya; taona, ali ku munda wamphesa wa Naboti kumene anatsikira kukaulandira.

19. Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, mulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agaru ananyambita mwazi wa Naboti, pompaja agaru adzanyambita mwazi wako, inde wako.

20. Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kucita coipaco pamaso pa Yehova.

21. Taona, ndidzakufikitsira coipa, ndi kucotsa mbumba yako psiti; ndipo ndidzalikhira Ahabu mwana wamwamuna yense, ndi yense womangika ndi womasuka m'lsrayeli;

22. ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi ya Basa mwana wa Ahiya; cifukwa ca kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kucimwitsa Israyeli.

23. Ndipo za Yezebeli yemwe Yehova ananena, nati, Agaru adzadya Yezebeli ku linga la Yezreeli.

24. Mwana ali yense wa Ahabu amene adzafera m'mudzi, agaru adzamudya; ndipo iye amene adzafera kuthengo, mbalame za m'mlengalenga zidzamudya,

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 21