Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 20:18-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Nati iye, Cinkana aturukira mumtendere, agwireni amoyo; cinkana aturukira m'nkhondo, agwireni amoyo.

19. Tsono anaturuka m'mudzi anyamata a akalonga a madera aja, ndi khamu la nkhondo linawatsata.

20. Ndipo ali yense anapha munthu wace; ndipo Aaramu anathawa, Aisrayeli nawapitikitsa; ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anathawira pa kavalo pamodzi ndi apakavalo.

21. Tsono mfumu ya Israyeli inaturuka, nikantha apakavalo ndi apamagareta, nawapha Aaramuwo maphedwe akuru.

22. Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israyeli, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe mucenjere ndi cimene mucicita; popeza caka cikudzaci mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu.

23. Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m'mene atilakira; koma tikaponyana nao kucidikha, zedi tidzaposa mphamvu.

24. Tsono citani ici, cotsani mafumu aja yense ku malo ace, muike m'malo mwao akazembe.

25. Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magareta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pacidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene.

26. Tsono kunacitika, pakufikanso caka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Meld kukaponyana ndi Aisrayeli.

27. Ndipo Aisrayeli anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisrayeli anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta ana a mbuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.

28. Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israyeli, nati, Atero: Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ici ndidzapereka unyinji uwu waukuru m'dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.

29. Ndipo awa anakhala m'misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israyeli anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi.

30. Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumudzi, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mudzi, m'cipinda ca m'katimo.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 20