Ndipo ali yense anapha munthu wace; ndipo Aaramu anathawa, Aisrayeli nawapitikitsa; ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anathawira pa kavalo pamodzi ndi apakavalo.