Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israyeli, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe mucenjere ndi cimene mucicita; popeza caka cikudzaci mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu.