Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 2:8-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo taona uli naye Simeyi mwana wa Gera wa pfuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikuru tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordano, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga,

9. Ndipo tsono, usamuyesera iye wosacimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumcitira iye, nutsitsire mutu wace waimvi ndi mwazi kumanda.

10. Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ace, naikidwa m'mudzi wa Davide.

11. Ndipo masiku ace akukhala Davide mfumu ya Israyeli anali zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu ku Hebroni, ndi zaka makumi atatu mphambu citatu anakhala mfumu ku Yerusalemu.

12. Tsono Solomo anakhala pa mpando wacifumu wa Davide atate wace, ndipo ufumu wace unakhazikika kwakukuru.

13. Pomwepo Adoniya mwana wa Hagati anadza kwa Batiseba amai wace wa Solomo, ndipo mkaziyo anati, Kodi wadza ndi mtendere? Nati, Ndi mtendere umene.

14. Anatinso, Ndiri nanu mau, Nati iye, Tanena.

15. Nati iye, Mudziwa kuti ufumu unali wanga, ndi kuti Aisrayeli onse anaika maso ao pa ine, kuti ndikhale mfumu ndine; koma ufumu watembenuka nukhala wa mbale wanga, popeza iye anaulandira kwa Mulungu.

16. Ndipo tsopano, ndikupemphani pempho limodzi, musandikaniza. Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Tanena.

17. Nati iye, Mundinenere kwa mfumu Solomo, popeza sakukanizani, kuti andipatse Abisagi wa ku Sunamu akhale mkazi wanga.

18. Ndipo Batiseba anati, Cabwino, ndidzakunenera kwa mfumu.

19. Tsono Batiseba ananka kwa mfumu Solomo kukanenera Adoniya kwa iye. Ndipo mfumu inanyamuka kukomana naye, namuweramira nakhalanso pa mpando wace wacifumu, naikitsa mpando wina wa amace wa mfumu, nakhala iye ku dzanja lace lamanja.

20. Pamenepo mkaziyo anati, Ndikupemphani kapempho kamodzi, musandikaniza. Ndipo mfumu inati kwa iye, Tapemphani amai wanga, popeza sindikukanizani.

21. Ndipo iye anati, Abisagi wa ku Sunamu apatsidwe kwa Adoniya mbale wanu akhale mkazi wace.

22. Ndipo mfumu Solomo anayankha, nati kwa amai wace, Mupempheranji Abisagi wa ku Sunamu akhale wace wa Adoniya? Mumpempherenso ufumu, popeza ndiye mkuru wanga; inde ukhale wace, ndi wa Abyatara wansembeyo, ndi wa Yoabu mwana wa Zeruya.

23. Pomwepo mfumu Solomo analumbira pa Yehova, nati, Mulungu andilange naonjezepo, zedi Adoniya wadziphetsa yekha ndi mau awa.

24. Ndipo tsono, pali Yehova amene wandikhazikitsa ine, nandikhalitsa pampando wacifumu wa Davide atate wanga, nandimangira nyumba monga analonjeza, zedi Adoniya aphedwa lero lomwe.

25. Ndipo mfumu Solomo anatuma dzanja la Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo anamgwera, namwalira iye.

26. Ndipo mfumu inanena ndi Abyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, cifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unazunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo.

27. Motero Solomo anacotsa Abyatara asakhalenso wansembe wa Yehova, kuti akakwaniritse mau a Yehova amene aja adalankhula ku Silo za mbumba ya Eli.

28. Ndipo mbiriyi inamfika Yoabu, pakuti Yoabu anapambukira kwa Adoniya, angakhale sanapambukira kwa Abisalomu. Ndipo Yoabu anathawira ku cihema ca Yehova, nagwira nyanga za guwa la nsembe.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 2