Koma ucitire zokoma ana amuna aja a Barizilai wa ku Gileadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.