Ndipo mfumu inanena ndi Abyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, cifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unazunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo.