Nati iye, Mudziwa kuti ufumu unali wanga, ndi kuti Aisrayeli onse anaika maso ao pa ine, kuti ndikhale mfumu ndine; koma ufumu watembenuka nukhala wa mbale wanga, popeza iye anaulandira kwa Mulungu.