Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 18:17-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo kunacitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye Kodi ndiwe uja umbvuta Israyeliyo?

18. Nati iye, Sindimabvuta Israyeli ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.

19. Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisrayeli onse ku phiri la Karimeli, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a cifanizoco mazana anai, akudya pa gome la Yezebeli.

20. Pamenepo Ahabu anatumiza mau kwa ana onse a Israyeli, namemeza aneneri onse ku phiri la Karimeli.

21. Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayika-kayika kufikira liti? ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo anthu nnena kumyankha mau amodzi.

22. Ndipo Eliya ananena ndi anthuwo, Ine ndatsala ndekha mneneri wa Yehova, koma aneneri a Baala ndiwo anthu mazana anai mphambu makumi asanu.

23. Atipatse tsono ng'ombe ziwiri; ndipo adzisankhire iwo eni ng'ombe imodzi, naiduledule, naiike pankhuni osasonkhapo moto; ndipo ine ndidzakonza ng'ombe yinayo, ndi kulika pankhuni osasonkhapo moto.

24. Ndipo muitane inu dzina la mulungu wanu, ine ndidzaitana dzina la Yehova; ndipo Mulunguyo ayankhe ndi mote ndiye Mulungu. Ndipo anthu onse anabvomera, nati, Ndiwo mau abwino amene.

25. Pamenepo Eliya ananena ndi aneneri a Paala, Dzisankhireni ng'ombe imodzi yanu, muyambe kuikonza, popeza mucuruka; nimuitane dzina la mulungu wanu, koma musasonkhepo moto.

26. Ndipo iwo anatenga ng'ombe ija adawapatsa, naikonza, naitana dzina la Baala, kuyambira m'mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wobvomereza. Ndipo anabvinabvina kuguwa adalimanga.

27. Ndipo pausana Eliya anawaseka, nati, Kwezani mau, popeza ndiye mulungu; kapena alikulingirira, kapena wapambuka, kapena ali paulendo, kaya agona, adzagalamuka.

28. Ndipo anakwezadi mau, nadzitema monga makhalidwe ao ndi mipeni ndi nthungo, kuti mwazi wao unali cucucu.

29. Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wobvomereza, kapena wakuwamvera.

30. Pamenepo Eliya ananena ndi anthu onse, Senderani kwa ine; ndipo onse anasendera kwa iye. Iye nakonza guwa la nsembe la Yehova lidagumukalo.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 18