Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 18:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo atapita masiku ambiri, mau a Yehova anafika kwa Eliya caka cacitatu, nati, Kadzionetse kwa Ahabu, ndipo ndidzatumiza mvula padziko.

2. Ndipo Eliya anamka kukadzionetsa kwa Ahabu. Ndipo njala inali yaikuru m'Samaria.

3. Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang'anira nyumba yace. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova;

4. pakuti pamene Yezebeli anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.

5. Ndipo Ahabu anati kwa Obadiya, Kayendere dziko lonse ku zitsime zonse zamadzi, ndi ku mitsinje yonse, kapena tikapeza msipu ndi kusunga moyo wa akavalo ndi nyuru, zingafe nyama zonse.

6. Tsono iwo awiri anagawana dziko kukaliyendera; Ahabu anadzera njira yace yekha, ndi Obadiya njira yina yekha.

7. Ndipo Obadiya ali m'njira, taona, Eliya anakomana naye; iye namdziwa, namgwadira, nati, Ndinu kodi mbuye wanga Eliya?

8. Ndipo anamyankha, nati, Ndine amene; kauze mbuye wako kuti Eliya wabwera,

9. Iye nati, Ndacimwanji kuti mupereka kapolo wanu m'dzanja la Ahabu kundipha?

10. Pali Yehova Mulungu wanu, ngati kuli mtundu umodzi wa anthu, kapena ufumu, kumene mbuye wanga sanatumako kukufunani, ndipo pakunena iwo, Palibe iye, analumbiritsa ufumu umene ndi mtundu umene kuti sanakupezani.

11. Ndipo tsopano mukuti, Kauze mbuye wako kuti Eliya wabwera.

12. Ndipo kudzacitika, ine ntakusiyani, mzimu wa Yehova udzakunyamulirani kosakudziwa ine, ndipo ine ntakauza Ahabu, ndipo akalephera kukupezani, adzandipha. Koma ine kapolo wanu ndimaopa Yehova kuyambira ubwana wanga.

13. Kodi sanakuuzani mbuye wanga cimene ndidacita m'kuwapha Yezebeli aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m'phanga, ndikuwadyetsa mkate ndi madzi?

14. Ndipo tsopano inu mukuti, Kauze mbuye wako Eliya wabwera, ndipo adzandipha.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 18